By Barnaba M Zingani
Ukaziputa limba ndi nkhani ya mtsikana zina lake, elise. Iye adaivutikila sukulu, Nkusankhidwa yekha m'kalasi mwawo kupita ku sekondale. Koma chifukwa cha munthu wina yemwe adabisala n'kuthandiza, iye adatenga pathupi n'kulephera kupita kusekondale.
Elise adabereka mwana wamwamuna. Poifunitsitsa sukulu, iye adakamusiya mwanayo kunkhalango. Mwa chisomo cha mlengi, mlenje wina adamutola, n'kukamulera. Adamuphunzitsa mwanayu, mpaka kupambana maphunziro ake akauchenjede. Mwana uja atakula n'kuyamba ntchito adadzazindikirana ndi mayi ake.
Stay updated with the latest books, offers, and news. Enter your email to subscribe to our newsletter.